Malaki 2:14 - Buku Lopatulika14 Koma mukuti, Chifukwa ninji? Chifukwa kuti Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unamchitira chosakhulupirika, chinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Koma mukuti, Chifukwa ninji? Chifukwa kuti Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unamchitira chosakhulupirika, chinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Mumafunsa kuti, “Chifukwa chake nchiyani?” Chifukwa chake nchakuti Chauta anali mboni ya chipangano chimene udachita ndi mkazi wako woyamba. Sudakhulupirike kwa iye, ngakhale iyeyo ndiye mnzako ndi mkazi wako potsata chipanganocho. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Inu mukufunsa kuti, “Chifukwa chake nʼchiyani?” Chifukwa chake nʼchakuti Yehova ndi mboni ya pangano limene unachita ndi mkazi wa unyamata wako, chifukwa sunakhulupirike kwa iye, ngakhale kuti iyeyo ndiye mnzako, ndi mkazi wako mwapangano. Onani mutuwo |