kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.
1 Akorinto 6:3 - Buku Lopatulika Kodi simudziwa kuti tidzaweruza angelo? Koposa kotani nanga zinthu za moyo uno? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi simudziwa kuti tidzaweruza angelo? Koposa kotani nanga zinthu za moyo uno? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi simukudziŵa kuti tidzaweruza angelo? Nanji zinthu za moyo wapansipano? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi simukudziwa kuti mudzaweruza angelo? Nanga bwanji zinthu za mʼmoyo uno! |
kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.
ndi mlandu unakomera opatulika a Wam'mwambamwamba, nifika nthawi yakuti ufumu unali wao wa opatulikawo.
Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:
Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;
Ndipo zija zinagwa kumingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.
Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo?
Kodi simudziwa kuti matupi anu ali ziwalo za Khristu? Chifukwa chake ndidzatenga ziwalo za Khristu kodi, ndi kuziyesa ziwalo za mkazi wachiwerewere? Msatero iai.
Kapena simudziwa kuti iye wophatikidwa ndi mkazi wachiwerewere ali thupi limodzi? Pakuti awiriwo, ati, adzakhala thupi limodzi.
Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.
Chifukwa chake, ngati muli nayo milandu ya zinthu za moyo uno, kodi muweruzitsa iwo amene ayesedwa achabe mu Mpingo?
Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikali.
pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, napita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalamatiya.
Pakuti ngati Mulungu sanalekerere angelo adachimwawo, koma anawaponya kundende nawaika kumaenje a mdima, asungike akaweruzidwe;
Angelonso amene sanasunge chikhalidwe chao choyamba, komatu anasiya pokhala paopao, adawasunga m'ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.