1 Akorinto 4:3 - Buku Lopatulika Koma kwa ine kuli kanthu kakang'ono ndithu kuti ndiweruzidwe ndi inu, kapena pa bwalo la munthu; koma sindiweruza ngakhale ndekha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma kwa ine kuli kanthu kakang'ono ndithu kuti ndiweruzidwe ndi inu, kapena pa bwalo la munthu; koma sindiweruza ngakhale ndekha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kunena za ine ndekha, ndilibe nazo kanthu ngati ndiweruzidwa ndi inu, kapenanso ndi bwalo lina lililonse la anthu. Ndiponsotu ngakhale mwiniwakene sindidziweruza ndekha ai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndilibe nazo kanthu ngati ndiweruzidwa ndi inu kapena khothi lina lililonse. Ndithu, inenso sindidziweruza ndekha. |
ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m'moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani.
Pakuti sindidziwa kanthu kakundipalamulitsa; koma m'menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye.
Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.