Ndipo anatimva mkazi wina dzina lake Lidia, wakugulitsa chibakuwa, wa kumzinda wa Tiatira, amene anapembedza Mulungu; mtima wake Ambuye anatsegula; kuti amvere zimene anazinena Paulo.
1 Akorinto 2:5 - Buku Lopatulika kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m'nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m'nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndinkachita zimenezi kuti chikhulupiriro chanu chisakhazikike pa nzeru za anthu, koma chikhazikike pa mphamvu za Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kuti chikhulupiriro chanu chisatsamire pa nzeru ya anthu koma pa mphamvu za Mulungu. |
Ndipo anatimva mkazi wina dzina lake Lidia, wakugulitsa chibakuwa, wa kumzinda wa Tiatira, amene anapembedza Mulungu; mtima wake Ambuye anatsegula; kuti amvere zimene anazinena Paulo.
Pakuti Khristu sananditume ine kubatiza, koma kulalikira Uthenga Wabwino, si mu nzeru ya mau, kuti mtanda wa Khristu ungayesedwe wopanda pake.
Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa mu ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.
Koma tili nacho chuma ichi m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife;
m'mau a choonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa zida za chilungamo kulamanja ndi kulamanzere,