Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.
1 Akorinto 11:3 - Buku Lopatulika Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ndifuna kuti mudziŵe kuti Khristu ndiye mutu wa mwamuna aliyense, mwamuna ndiye mutu wa mkazi, ndipo Mulungu ndiye mutu wa Khristu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano ndikufuna muzindikire kuti Khristu ndiye mutu wa munthu aliyense, ndipo mwamuna ndiye mutu wamkazi, ndipo mutu wa Khristu ndi Mulungu. |
Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.
Taonani, Mtumiki wanga adzachita mwanzeru; adzakwezedwa ndi kutukulidwa pamwamba, nadzakhala pamwambamwamba.
Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.
Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; pakuti Atate ali wamkulu ndi Ine.
koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu;
Ndipo Iye ali mutu wa thupi, Mpingowo; ndiye chiyambi, wobadwa woyamba wotuluka mwa akufa; kuti akakhale Iye mwa zonse woyambayamba.
kuchokera kwa Iye amene thupi lonse, lothandizidwa ndi kulumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempha, likula ndi makulidwe a Mulungu.
Momwemonso, akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mau, akakodwe opanda mau mwa mayendedwe a akazi;