Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Akolose 3:18 - Buku Lopatulika

18 Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Inu akazi, gonjerani amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.

Onani mutuwo Koperani




Akolose 3:18
12 Mawu Ofanana  

Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.


Ndipo mau amene adzaika mfumu akamveka mu ufumu wake wonse, (pakuti ndiwo waukulu), akazi onse adzachitira amuna ao ulemu, aakulu ndi aang'ono.


Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.


Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.


Akazi akhale chete mu Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula. Koma akhale omvera, monganso chilamulo chinena.


Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye.


Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;


pakuti chipatso cha kuunika tichipeza mu ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi choonadi,


Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale chete.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa