Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa

Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano


Masalimo 23 - Buku Lopatulika Buku Lopatulika
Masalimo 23

Amwai amene Yehova akhala Mbusa wao
Salimo la Davide.

1 Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa.

2 Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha.

3 Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.

4 Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.

5 Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.

6 Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala m'nyumba ya Yehova masiku onse.

Bible Society of Malawi

Bible Society of Malawi