Masalimo 134 - Buku Lopatulika Buku Lopatulika Masalimo 134Afulumizidwa anthu kulemekeza YehovaNyimbo yokwerera.1 Taonani, lemekezani Yehova, atumiki a Yehova inu nonse, akuimirira m'nyumba ya Yehova usiku. 2 Kwezani manja anu kumalo oyera, nimulemekeze Yehova. 3 Yehova, ali mu Ziyoni, akudalitseni; ndiye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi. |