Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 26:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Kotero mu zigwa za Mowabu pafupi ndi mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, Mose ndi wansembe Eliezara anayankhula nawo kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Pamenepo Mose ndi Eleazara wansembe ananena nao m'zidikha za Mowabu pa Yordani kufupi ku Yeriko, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pamenepo Mose ndi Eleazara wansembe ananena nao m'zidikha za Mowabu pa Yordani kufupi ku Yeriko, ndi kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono Mose ndi wansembe Eleazara adalankhula ndi atsogoleri m'zigwa za ku Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani ku Yeriko, adati,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 26:3
10 Mawu Ofanana  

Aisraeli anayenda kupita ku zigwa za Mowabu nakamanga misasa yawo tsidya lina la Yorodani moyangʼanana ndi Yeriko.


“Werengani amuna a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo, monga momwe Yehova walamulira Mose.” Aisraeli omwe anachokera ku Igupto ndi awa:


Awa ndi amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eliezara wansembe pamene ankawerenga Aisraeli pa zigwa za ku Mowabu mʼmbali mwa Yorodani ku Yeriko.


Ndipo anabwera nawo akapolowo ndi zolanda ku nkhondozo kwa Mose ndi kwa wansembe Eliezara ndi kwa gulu lonse la Aisraeli ku misasa yawo ku chigwa cha Mowabu, mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko.


Atachoka ku mapiri a Abarimu anakamanga ku zigwa za Mowabu mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi Yeriko.


Ku zigwa za Mowabu pafupi ndi Yorodani ku Yeriko, Yehova anawuza Mose kuti,


Ndipo Mose anakwera Phiri la Nebo kuchokera ku chigwa cha Mowabu ndi kukafika pamwamba pa Phiri la Pisiga, kummawa kwa Yeriko. Kumeneko Yehova anamuonetsa dziko lonse; kuchokera ku Giliyadi mpaka ku Dani.


Yehova anamuyika mʼmanda ku Mowabu, mʼchigwa choyangʼanana ndi Beti-Peori, koma mpaka lero palibe amene amadziwa pamene pali manda ake.


Aisraeli analira maliro a Mose mʼchikhwawa cha Mowabu kwa masiku makumi atatu mpaka nthawi ya kulira maliro ndi kukhuza inatha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa