Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 26:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 “Werengani amuna a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo, monga momwe Yehova walamulira Mose.” Aisraeli omwe anachokera ku Igupto ndi awa:

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Awawerenge kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu; monga Yehova anawauza Mose ndi ana a Israele, amene adatuluka m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Awawerenge kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu; monga Yehova anawauza Mose ndi ana a Israele, amene adatuluka m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 “Muchite chiŵerengero cha anthu, kuyambira a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo,” monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Aisraele amene adatuluka m'dziko la Ejipito anali aŵa:

Onani mutuwo Koperani




Numeri 26:4
6 Mawu Ofanana  

Nawa ana a Israeli (ndiye kuti Yakobo ndi ana ake) amene anapita ku Igupto: Rubeni mwana woyamba wa Yakobo.


Satana anafuna kuvutitsa Aisraeli choncho anawutsa mtima wa Davide kuti awerenge Aisraeli.


Ndipo tsiku lomwelo Yehova anatulutsa gulu lonse la ana a Israeli mʼdziko la Igupto.”


Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai, mu tenti ya msonkhano, pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, mʼchaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, kuti,


Kotero mu zigwa za Mowabu pafupi ndi mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, Mose ndi wansembe Eliezara anayankhula nawo kuti,


Zidzukulu za Rubeni, mwana woyamba wamwamuna wa Israeli, zinali izi: kuchokera mwa Hanoki, fuko la Ahanoki; kuchokera mwa Palu, fuko la Apalu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa