Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 6:5 - Buku Lopatulika

5 Masiku onse a chowinda chake chakusala, lumo lisapite pamutu pake; kufikira adatha masikuwo adadzipatulira kwa Yehova, azikhala wopatulika; aleke nzera za tsitsi lake zimeretu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Masiku onse a chowinda chake chakusala, lumo lisapite pamutu pake; kufikira adatha masikuwo adadzipatulira kwa Yehova, azikhala wopatulika; aleke nzera za tsitsi lake zimeretu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 “Pa masiku onse amene adalumbira kuti adzakhala wodzipereka kwa Chauta, asamete kumutu kwake ndi lumo. Adzakhale wake wa Chauta nthaŵi zonse mpaka atatha masiku ake odzipereka kwa Chauta. Alilekerere tsitsi lake kuti likule.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 “ ‘Pa nthawi yonse ya lonjezo lodzipatula yekhalo, asamete kumutu kwake ndi lumo. Akhale wopatulika mpaka nthawi yake yonse ya kudzipatula yekha kwa Yehova itatha. Alileke tsitsi la pamutu pake kuti likule.’

Onani mutuwo Koperani




Numeri 6:5
9 Mawu Ofanana  

Ndipo asamete mitu yao, kapena asalekerere nzera za tsitsi lao zikule, azingoyepula tsitsi la mitu yao.


Masiku onse a kusala kwake asadye kanthu kopangika ndi mphesa, kuyambira nthanga zake kufikira khungu lake.


Paulo atakhala chikhalire masiku ambiri, anatsazika abale, nachoka pamenepo, napita m'ngalawa ku Siriya, pamodzi naye Prisila ndi Akwila; popeza anameta mutu wake mu Kenkrea; pakuti adawinda.


pakuti taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pake sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israele m'dzanja la Afilisti.


Pomwepo anamfotokozera mtima wake wonse, nanena naye, Pamutu panga sipanapite lumo, pakuti ndine Mnaziri wa Mulungu chiyambire mimba ya mai wanga; akandimeta, mphamvu yanga idzandichokera, ndidzakhala wofooka wakunga munthu wina aliyense.


Pamenepo anamgonetsa pa mabondo ake, naitana munthu, nameta njombi zake zisanu ndi ziwiri; nayamba kumzunza, nimchokera mphamvu yake.


nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa