Numeri 6:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 “ ‘Pa nthawi yonse ya lonjezo lodzipatula yekhalo, asamete kumutu kwake ndi lumo. Akhale wopatulika mpaka nthawi yake yonse ya kudzipatula yekha kwa Yehova itatha. Alileke tsitsi la pamutu pake kuti likule.’ Onani mutuwoBuku Lopatulika5 Masiku onse a chowinda chake chakusala, lumo lisapite pamutu pake; kufikira adatha masikuwo adadzipatulira kwa Yehova, azikhala wopatulika; aleke nzera za tsitsi lake zimeretu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Masiku onse a chowinda chake chakusala, lumo lisapite pamutu pake; kufikira adatha masikuwo adadzipatulira kwa Yehova, azikhala wopatulika; aleke nzera za tsitsi lake zimeretu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 “Pa masiku onse amene adalumbira kuti adzakhala wodzipereka kwa Chauta, asamete kumutu kwake ndi lumo. Adzakhale wake wa Chauta nthaŵi zonse mpaka atatha masiku ake odzipereka kwa Chauta. Alilekerere tsitsi lake kuti likule. Onani mutuwo |
chifukwa mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo akadzabadwa lumo lisadzapite pa mutu chifukwa mnyamatayo adzakhala Mnaziri, ndiye kuti wopatulika kwa Mulungu kuyambira pa nthawi imene adzakhale ali mʼchiberekero. Ndipo adzayamba ntchito yopulumutsa Israeli mʼmanja mwa Afilisti.”