Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 22:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Mowabu anati kwa akulu a Midiyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse zili pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Mowabu masiku amenewo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Mowabu anati kwa akulu a Midiyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse zili pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Mowabu masiku amenewo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Choncho Amowabuwo adauza akuluakulu a ku Midiyani kuti, “Tsopano khamu limeneli libudula zonse zimene zatizungulira, monga momwe ng'ombe zimabudulira udzu wam'munda.” Pamenepo Balaki mwana wa Zipori amene anali mfumu ya Mowabu nthaŵi imeneyo,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Iwo anati kwa akuluakulu a ku Midiyani, “Gulu ili lidzabudula zonse zimene zatizungulira monga momwe ngʼombe yothena imathera udzu wa ku tchire.” Tsono Balaki mwana wa Zipori, yemwe anali mfumu ya Mowabu pa nthawi imeneyo,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 22:4
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anachoka ku Midiyani nafika ku Parani, natenga anthu a ku Parani pamodzi nao, nafika ku Ejipito kwa Farao mfumu ya Aejipito, ameneyo anampatsa nyumba, namnenera zakudya, nampatsako dziko.


Pamenepo mafumu a Edomu anadabwa; agwidwa nako kunthunthumira amphamvu a ku Mowabu; okhala mu Kanani onse asungunuka mtima.


Pamwamba pa matsindwi a Mowabu ndi m'miseu mwake muli kulira monsemonse; pakuti ndaswa Mowabu monga mbiya m'mene mulibe chikondwero, ati Yehova.


Ndipo Balaki mwana wa Zipori anaona zonse Israele anachitira Aamori.


Ndipo akulu a Mowabu ndi akulu a Midiyani anamuka ndi mphotho za maula m'dzanja lao; anadza kwa Balamu, nanena naye mau a Balaki.


Ndimuona, koma tsopano ai; ndimpenya, koma si pafupi ai; idzatuluka nyenyezi mu Yakobo, ndi ndodo yachifumu idzauka mu Israele, nidzakantha malire a Mowabu, nidzapasula ana onse a Seti.


Ndipo, taonani, anadza wina wa ana a Israele, nabwera naye mkazi Mmidiyani kudza naye kwa abale ake, pamaso pa Mose, ndi pamaso pa khamu lonse la ana a Israele, pakulira iwo pa khomo la chihema chokomanako.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


Ndipo anapha mafumu a Amidiyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidiyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga.


Ndipo tsopano kodi inu ndinu wabwino woposa Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu; anatengana konse ndi Israele iyeyu kodi, kapena kuchita nao nkhondo konse kodi?


Koma ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Midiyani zaka zisanu ndi ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa