Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 22:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Iwo anati kwa akuluakulu a ku Midiyani, “Gulu ili lidzabudula zonse zimene zatizungulira monga momwe ngʼombe yothena imathera udzu wa ku tchire.” Tsono Balaki mwana wa Zipori, yemwe anali mfumu ya Mowabu pa nthawi imeneyo,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ndipo Mowabu anati kwa akulu a Midiyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse zili pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Mowabu masiku amenewo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Mowabu anati kwa akulu a Midiyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse zili pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Mowabu masiku amenewo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Choncho Amowabuwo adauza akuluakulu a ku Midiyani kuti, “Tsopano khamu limeneli libudula zonse zimene zatizungulira, monga momwe ng'ombe zimabudulira udzu wam'munda.” Pamenepo Balaki mwana wa Zipori amene anali mfumu ya Mowabu nthaŵi imeneyo,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 22:4
13 Mawu Ofanana  

Iwo ananyamuka ku Midiya ndi kupita ku Parani. Ndipo anatenga amuna ena ku Paraniko, napita nawo ku Igupto, kwa Farao mfumu ya Igupto, amene anamupatsa nyumba, malo ndiponso chakudya.


Tsopano mafumu a ku Edomu agwidwa ndi mantha aakulu, otsogolera a dziko la Mowabu akunjenjemera ndi mantha, ndipo anthu a ku Kanaani asungunuka ndi mantha.


Pa madenga onse a ku Mowabu ndiponso mʼmisewu yake anthu akungolira, pakuti ndaphwanya Mowabu ngati mtsuko wopanda ntchito,” akutero Yehova.


Tsono Balaki mwana wa Zipori anaona zonse zimene Aisraeli anachitira Aamori,


Akuluakulu a Mowabu ndi akuluakulu a Midiyani ananyamuka atatenga ndalama zokalipirira mawula. Atafika kwa Balaamu, anamuwuza zomwe Balaki ananena.


“Ndikumuona iye koma osati tsopano; ndikumupenya iye koma osati pafupi. Nyenyezi idzatuluka mwa Yakobo; ndodo yaufumu idzatuluka mwa Israeli. Iye adzagonjetsa Mowabu ndi kugonjetsa ana onse a Seti.


Kenaka mwamuna wina wa ku Israeli anabweretsa ku banja lake mkazi wa Chimidiyani pamaso pa Mose ndi anthu onse a Israeli pamene ankalira pa khomo la tenti ya msonkhano.


Yehova anawuza Mose kuti,


Mwa anthu ophedwawo munali Evi, Rekemu, Zuri, Huri ndi Reba, mafumu asanu a Amidiyani. Ndipo anaphanso ndi lupanga Balaamu mwana wa Beori.


Kodi ndinu abwino kuposa Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu? Kodi iye anakanganapo kapena kuchita nkhondo ndi Israeli?


Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova, choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Amidiyani kwa zaka zisanu ndi ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa