Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 22:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo anatuma amithenga kwa Balamu mwana wa Beori, ku Petori, wokhala kumtsinje, wa dziko la anthu a mtundu wake, kuti amuitane, ndi kuti, Taonani, anatuluka anthu m'dziko la Ejipito; taonani, aphimba nkhope ya dziko, nakhala popenyana ndi ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo anatuma amithenga kwa Balamu mwana wa Beori, ku Petori, wokhala kumtsinje, wa dziko la anthu a mtundu wake, kuti amuitane, ndi kuti, Taonani, anatuluka anthu m'dziko la Ejipito; taonani, aphimba nkhope ya dziko, nakhala popenyana ndi ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 adatuma amithenga kwa Balamu, mwana wa Beori, ku Petori, pafupi ndi mtsinje wa Yufurate m'dziko la kwao, kuti akamuitane ndi kumuuza kuti, “Anthu ochokera ku Ejipito adzaza dziko lonse, ndipo akuyang'anana ndi ine.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 anatumiza amithenga kwa Balaamu mwana wa Beori, yemwe anali ku Petori, pafupi ndi mtsinje, mʼdziko la kwawo kuti akamuyitane. Balaki anati: “Taonani, anthu ochokera ku Igupto abwera, adzaza dziko lonse ndipo akufuna kuchita nane nkhondo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 22:5
15 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzayesa mbeu yako monga fumbi lapansi: chotere kuti ngati munthu angathe kuwerenga fumbi lapansi, chomwechonso mbeu yako idzawerengedwa.


Ndipo anachulukitsatu mtundu wa anthu ake, nawapatsa mphamvu yoposa owasautsa.


Pakuti linakuta nkhope ya dziko lonse kuti dziko linada; ndipo linadya zitsamba zonse za m'dziko, ndi zipatso zonse za mitengo zimene matalala adazisiya; ndipo sipanatsale chabiriwiri chilichonse, pamitengo kapena pa zitsamba zakuthengo, m'dziko lonse la Ejipito.


Anthu anga, kumbukiranitu chofunsira Balaki mfumu ya Mowabu, ndi chomuyankha Balamu mwana wa Beori, kuyambira ku Sitimu kufikira ku Giligala; kuti mudziwe zolungama za Yehova.


Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ku Aramu ananditenga Balaki, mfumu ya Mowabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa, Idza, udzanditembererere Yakobo. Idza, nudzanyoze Israele.


Ndipo anapha mafumu a Amidiyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidiyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga.


popeza sanakumane nanu ndi mkate ndi madzi m'njira muja munatuluka mu Ejipito; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesopotamiya, kuti akutemberereni.


Ndipo Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu; koma Yehova Mulungu wanu anakusandulizirani tembererolo likhale mdalitso, popeza Yehova Mulungu wanu anakukondani.


Ana a Israele anaphanso ndi lupanga Balamu mwana wa Beori, mlauli uja, pamodzi ndi ena adawaphawo.


Pamenepo Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, anauka naponyana ndi Israele; natuma naitana Balamu mwana wa Beori atemberere inu;


Tsoka kwa iwo! Pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m'chitsutsano cha Kora.


Komatu ndili nazo zinthu pang'ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israele, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nachite chigololo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa