Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 22:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo tsopano, idzatu, nunditembererere anthu awa; popeza andiposa mphamvu; kapena ndidzawapambana, kuti tiwakanthe, ndi kuti ndiwapirikitse m'dziko; pakuti ndidziwa kuti iye amene umdalitsa adalitsika, ndi iye amene umtemberera atemberereka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo tsopano, idzatu, nunditembererere anthu awa; popeza andiposa mphamvu; kapena ndidzawapambana, kuti tiwakanthe, ndi kuti ndiwapirikitse m'dziko; pakuti ndidziwa kuti iye amene umdalitsa adalitsika, ndi iye amene umtemberera atemberereka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Bwerani tsono muŵatemberere anthu ameneŵa m'malo mwanga, poti ngamphamvu kopambana ine. Mwina mwake ndidzatha kuŵagonjetsa ndi kuŵapirikitsa m'dziko mwanga. Pakuti ndikudziŵa kuti amene inu mumamdalitsa, amadalitsidwa, ndipo amene mumamtemberera, amatembereredwa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Tsopano bwera, utemberere anthu amenewa chifukwa ndi amphamvu kwambiri kuposa ine. Mwina ndingadzawagonjetse ndi kuwatulutsira kunja kwa dzikoli chifukwa ndikudziwa kuti amene umawadalitsa amadalitsika, ndipo amene umawatemberera amatembereredwa.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 22:6
23 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.


Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.


Tsono mthenga uja udakaitana Mikaya unanena naye, nati, Taona, mau a aneneri avomerezana zokoma kwa mfumu ndi m'kamwa mmodzi; mau ako tsono afanane ndi mau a wina wa iwowo, nunene zabwino.


Pamenepo mfumu ya Israele inasonkhanitsa aneneri ngati anthu mazana anai, nanena nao, Kodi ndizimuka kukathira nkhondo pa Ramoti Giliyadi, kapena ndileke? Nati iwo, Kweraniko; popeza Ambuye adzaupereka m'dzanja la mfumu.


Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wake wa Imila. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu.


popeza sanawachingamire ana a Israele ndi chakudya ndi madzi, koma anawalemberera Balamu awatemberere; koma Mulungu wathu anasanduliza tembererolo likhale mdalitso.


Atemberere iwowa, koma mudalitse ndinu; pakuuka iwowa adzachita manyazi, koma mtumiki wanu adzakondwera.


Monga mpheta ilikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka, momwemo temberero la pachabe silifikira.


Iwo aona zopanda pake, ndi phenda labodza amene anena, Atero Yehova; koma Yehova sanawatume, nayembekezetsa anthu kuti mauwo adzakhazikika.


Anthu anga, kumbukiranitu chofunsira Balaki mfumu ya Mowabu, ndi chomuyankha Balamu mwana wa Beori, kuyambira ku Sitimu kufikira ku Giligala; kuti mudziwe zolungama za Yehova.


Koma Mulungu anati kwa Balamu, Usapita nao; usatemberera anthuwa; pakuti adalitsika.


popeza ndidzakuchitira ulemu waukulu, ndipo zonse unena ndi ine ndidzachita; chifukwa chake idzatu, unditembererere anthu awa.


Ndipo Balaki anati naye, Tiyetu, upite nane kumalo kwina, kumene ukawaona; udzaona malekezero ao okha, osawaona onse; ndipo pokhala pamenepo ukanditembererere iwo.


Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Tiyetu, ndimuke nawe kumalo kwina; kapena kudzakomera pamaso pa Mulungu kuti unditembererere iwo pokhala kumeneko.


Anaunthama, nagona pansi ngati mkango, ngati mkango waukazi; adzamuutsa ndani? Wodalitsika aliyense wakudalitsa iwe, wotemberereka aliyense wakutemberera iwe.


Ndipo panali, pamene tinali kunka kukapemphera, anakomana ndi ife mdzakazi wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ake zambiri pakubwebweta pake.


popeza sanakumane nanu ndi mkate ndi madzi m'njira muja munatuluka mu Ejipito; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesopotamiya, kuti akutemberereni.


Pamenepo Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, anauka naponyana ndi Israele; natuma naitana Balamu mwana wa Beori atemberere inu;


Ndipo Mfilisti anati kwa Davide, Ine ndine galu kodi, kuti iwe ukudza kwa ine ndi ndodo? Ndi Mfilistiyo anatukwana Davide natchula milungu yake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa