Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 22:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo akulu a Mowabu ndi akulu a Midiyani anamuka ndi mphotho za maula m'dzanja lao; anadza kwa Balamu, nanena naye mau a Balaki.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo akulu a Mowabu ndi akulu a Midiyani anamuka ndi mphotho za maula m'dzanja lao; anadza kwa Balamu, nanena naye mau a Balaki.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Choncho akalonga a ku Mowabu ndi akalonga a ku Midiyani adanyamuka, atatenga ndalama m'manja zokaombedzera. Tsono adafika kwa Balamu namuuza mau a Balaki.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Akuluakulu a Mowabu ndi akuluakulu a Midiyani ananyamuka atatenga ndalama zokalipirira mawula. Atafika kwa Balaamu, anamuwuza zomwe Balaki ananena.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 22:7
15 Mawu Ofanana  

Akulu ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera milandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika.


Inde agalu ali osusuka, sakhuta konse; amenewa ali abusa osazindikira; iwo onse atembenukira kunjira zao, yense kutsata phindu lake m'dera lake.


Ndipo mundidetsa mwa anthu anga kulandirapo barele wodzala manja, ndi zidutsu za mkate, kuipha miyoyo yosayenera kufa, ndi kusunga miyoyo yosayenera kukhala ndi moyo, ndi kunena mabodza kwa anthu anga omvera bodza.


Pakuti mfumu ya ku Babiloni aima pa mphambano ya njira, polekana njira ziwirizo, kuti aombeze maula; agwedeza mivi, afunsira kwa aterafi, apenda ndi chiwindi.


Akulu ake aweruza chifukwa cha mphotho, ndi ansembe ake aphunzitsa chifukwa cha malipo, ndi aneneri ake alosa chifukwa cha ndalama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? Palibe choipa chodzatigwera.


Ndipo ananena nao, Mugone kuno usiku uno, ndidzakubwezerani mau, monga Yehova adzanena ndi ine; pamenepo mafumu a Mowabu anagona ndi Balamu.


Pakuti palibe nyanga pakati pa Yakobo, kapena ula mwa Israele; pa nyengo yake adzanena kwa Yakobo ndi Israele, chimene Mulungu achita.


Pamene Balamu anaona kuti kudakomera pamaso pa Yehova kudalitsa Israele, sanamuke, monga nthawi zina zija, ku nyanga zolodzera, koma anayang'ana nkhope yake kuchipululu.


Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.


amene ayenera kutsekedwa pakamwa; ndiwo amene apasula mabanja banja lonse, ndi kuphunzitsa zosayenera chifukwa cha chisiriro chonyansa.


Ana a Israele anaphanso ndi lupanga Balamu mwana wa Beori, mlauli uja, pamodzi ndi ena adawaphawo.


posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya chosalungama;


Tsoka kwa iwo! Pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m'chitsutsano cha Kora.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa