Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 21:1 - Buku Lopatulika

1 Pamene Mkanani, mfumu ya Aradi, wokhala kumwera, anamva kuti Israele anadzera njira ya Atarimu, anathira nkhondo pa Israele, nagwira ena akhale ansinga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pamene Mkanani, mfumu ya Aradi, wokhala kumwera, anamva kuti Israele anadzera njira ya Atarimu, anathira nkhondo pa Israele, nagwira ena akhale ansinga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mfumu Yachikanani ya ku Aradi imene inkakhala kumwera, itamva kuti Aisraele akubwera, kudzera njira ya ku Atarimu, idathira nkhondo Aisraelewo, nigwirako ena ukapolo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mfumu ya Akanaani ya ku Aradi, imene inkakhala ku Negevi, itamva kuti Aisraeli akubwera kudzera msewu wopita ku Atarimu, inachita nkhondo ndi Aisraeli nigwira ena mwa iwo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 21:1
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anayenda ulendo wake, nayendayenda kunka kumwera.


Pamenepo anatsika Aamaleke, ndi Akanani, akukhala m'phirimo nawakantha, nawapha kufikira ku Horoma.


Ndipo Mkanani, mfumu ya Aradi, wakukhala kumwera m'dziko la Kanani, anamva za kudza kwao kwa ana a Israele.


Pamenepo Sihoni anatuluka kukomana nafe, iye ndi anthu ake onse, kumenyana nafe nkhondo ku Yahazi.


mfumu ya ku Horoma, imodzi; mfumu ya ku Aradi, imodzi;


Ndipo amuna a ku Ai anawakantha amuna, ngati makumi atatu mphambu asanu ndi mmodzi; nawapirikitsa kuyambira pachipata mpaka ku Sebarimu, nawakantha potsika; ndi mitima ya anthu inasungunuka inga madzi.


Ndipo ana a Mkeni mlamu wake wa Mose, anakwera kutuluka m'mzinda wa m'migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m'chipululu cha Yuda chokhala kumwera kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa