Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 21:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Israele analonjeza chowinda kwa Yehova, nati, Mukadzaperekatu anthu awa m'dzanja langa, ndidzaononga mizinda yao konse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Israele analonjeza chowinda kwa Yehova, nati, Mukadzaperekatu anthu awa m'dzanja langa, ndidzaononga midzi yao konse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsono Aisraele adalumbira kwa Chauta kuti, “Ngati muŵapereka anthu ameneŵa m'manja mwathu, ife tidzaonongeratu mizinda yao.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndipo Israeli anachita lonjezo ili kwa Yehova: “Mukapereka anthu awa mʼdzanja lathu ife tidzawonongeratu mizinda yawo.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 21:2
15 Mawu Ofanana  

Yakobo ndipo analumbira chilumbiro, nati, Mulungu akakhala ndi ine, akandisunga ine m'njira imene ndipitamo, akandipatsa ine mkate wa kudya, ndi zovalira za kuvala,


Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova, tsopano, pamaso pa anthu ake onse.


Kuti analumbira Yehova, nawindira Wamphamvuyo wa Yakobo, ndi kuti,


Ngati wina sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Akudza Ambuye.


muzikanthatu okhala m'mzinda muja ndi lupanga lakuthwa; ndi kuononga konse, ndi zonse zili m'mwemo, ng'ombe zake zomwe, ndi lupanga lakuthwa.


Ndipo muzikundika zofunkha zake zonse pakati pakhwalala pake, nimutenthe ndi moto mzinda, ndi zofunkha zake zonse konse, pamaso pa Yehova Mulungu wanu; ndipo udzakhala mulu ku nthawi zonse; asaumangenso.


Koma za mizinda ya amitundu awa, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ikhale cholowa chanu, musasiyepo chamoyo chilichonse chakupuma;


nakawapereka Yehova Mulungu wanu pamaso panu, ndipo mukawakanthe; pamenepo muwaononge konse; musapangana nao pangano, kapena kuwachitira chifundo.


Koma mzindawo udzaperekedwa kwa Yehova ndi kuonongeka konse, uwu ndi zonse zili m'mwemo; Rahabi yekha wadamayo adzakhala ndi moyo, iye ndi onse ali naye m'nyumba, chifukwa anabisa mithenga tinawatumawo.


Ndipo Yoswa anawalumbirira nyengo ija, ndi kuti, Wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzauka ndi kumanga mzinda uwu wa Yeriko; adzamanga maziko ake ndi kutayapo mwana wake woyamba, nadzaimika zitseko zake ndi kutayapo mwana wake wotsirizira.


Ndipo Yefita anawindira Yehova chowinda, nati, Mukaperekatu ana a Amoni m'dzanja langa,


nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa