Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 27:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo m'kupingasa kwa bwaloli pa mbali ya kumadzulo mukhale nsalu zotchingira za mikono makumi asanu; nsichi zake zikhale khumi, ndi makamwa ao khumi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo m'kupingasa kwa bwaloli pa mbali ya kumadzulo mukhale nsalu zochingira za mikono makumi asanu; nsichi zake zikhale khumi, ndi makamwa ao khumi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Muufupi mwake mwa bwalolo cha mbali yakuzambwe, pakhale nsalu zochinga, kutalika kwake mamita 23, ndi nsanamira khumi ndi masinde khumi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “Mbali yakumadzulo ya bwalolo ikhale yotalika mamita 23 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga, nsichi khumi ndi matsinde khumi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 27:12
4 Mawu Ofanana  

Nuzipanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri;


Momwemonso pa mbali ya ku kumpoto mu utali mwake pakhale nsalu zotchingira za mikono zana limodzi mu utali mwake; ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao akhale amkuwa; zokowera za nsichizo ndi mitanda yake zikhale zasiliva.


Ndipo m'kupingasa kwake kwa bwalo pa mbali ya kum'mawa, kum'mawa, mukhale mikono makumi asanu.


ndi nsalu zotchinga za kubwalo, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, lokhala ku chihema, ndi ku guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zake za ku ntchito zake zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa