Eksodo 27:11 - Buku Lopatulika11 Momwemonso pa mbali ya ku kumpoto mu utali mwake pakhale nsalu zotchingira za mikono zana limodzi mu utali mwake; ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao akhale amkuwa; zokowera za nsichizo ndi mitanda yake zikhale zasiliva. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Momwemonso pa mbali ya ku kumpoto m'utali mwake pakhale nsalu zochingira za mikono zana limodzi m'utali mwake; ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao akhale amkuwa; zokowera za nsichizo ndi mitanda yake zikhale zasiliva. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Momwemonso pa mbali yakumpoto, uike nsalu zochinga, kutalika kwake mamita 46, ndi nsanamira zamkuŵa makumi aŵiri. Nsanamirazo zimangidwe pa masinde ake makumi aŵiri, koma ngoŵe za nsanamirazo ndi mitanda yake zikhale zasiliva. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Mbali yakumpoto ikhalenso yotalika mamita 46 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga. Pakhalenso mizati makumi awiri, matsinde amkuwa makumi awiri, ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. Onani mutuwo |