Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 27:11 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Mbali yakumpoto ikhalenso yotalika mamita 46 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga. Pakhalenso mizati makumi awiri, matsinde amkuwa makumi awiri, ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

11 Momwemonso pa mbali ya ku kumpoto mu utali mwake pakhale nsalu zotchingira za mikono zana limodzi mu utali mwake; ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao akhale amkuwa; zokowera za nsichizo ndi mitanda yake zikhale zasiliva.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Momwemonso pa mbali ya ku kumpoto m'utali mwake pakhale nsalu zochingira za mikono zana limodzi m'utali mwake; ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao akhale amkuwa; zokowera za nsichizo ndi mitanda yake zikhale zasiliva.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Momwemonso pa mbali yakumpoto, uike nsalu zochinga, kutalika kwake mamita 46, ndi nsanamira zamkuŵa makumi aŵiri. Nsanamirazo zimangidwe pa masinde ake makumi aŵiri, koma ngoŵe za nsanamirazo ndi mitanda yake zikhale zasiliva.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 27:11
2 Mawu Ofanana  

Upangenso mizati makumi awiri, matsinde makumi awiri amkuwa, ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo.


“Mbali yakumadzulo ya bwalolo ikhale yotalika mamita 23 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga, nsichi khumi ndi matsinde khumi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa