Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 15:5 - Buku Lopatulika

5 Nyanja inawamiza; anamira mozama ngati mwala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Nyanja inawamiza; anamira mozama ngati mwala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Nyanja yozamayo idaŵaphimba onse, adamira mpaka pansi pa nyanja ngati miyala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Nyanja yakuya inawaphimba; Iwo anamira pansi ngati mwala.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 15:5
12 Mawu Ofanana  

Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba.


Ndipo madziwo anamiza owasautsa; sanatsale mmodzi yense.


Popeza madziwo anabwerera, namiza magaleta ndi apakavalo, ndiwo nkhondo yonse ya Farao imene idalowa pambuyo pao m'nyanja; sanatsale wa iwowa ndi mmodzi yense.


Munaombetsa mphepo yanu, nyanja inawamiza; anamira m'madzi aakulu ngati mtovu.


Kuopa kwakukulu ndi mantha ziwagwera; padzanja lanu lalikulu akhala chete ngati mwala; kufikira apita anthu anu, Yehova, kufikira apita anthu amene mudawaombola.


Pamene panalibe zozama ndinabadwa ine, pamene panalibe akasupe odzala madzi.


Muja unathyoka ndi nyanja m'madzi akuya malonda ako ndi msonkhano wako wonse adagwa pakati pako.


Ndipo anati, Ndinaitana Yehova m'nsautso wanga, ndipo anandiyankha ine; ndinafuula ndili m'mimba ya manda, ndipo munamva mau anga.


Adzabwera, nadzatichitira nsoni; adzagonjetsa mphulupulu zathu; ndipo mudzataya zochimwa zao zonse m'nyanja yakuya.


koma yense amene adzakhumudwitsa kamodzi ka tiana iti, takukhulupirira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yaikulu ikolowekedwe m'khosi mwake, namizidwe poya pa nyanja.


Ndipo mngelo wolimba ananyamula mwala ngati mphero yaikulu, naiponya m'nyanja, nanena, Chotero Babiloni, mzinda waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa