Danieli 4:25 - Buku Lopatulika25 kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, ndipo zidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201425 kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, nizidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero25 Inu mudzachotsedwa pakati pa anthu ndipo mudzakhala ndi nyama zakuthengo; mudzadya udzu monga ngʼombe ndi kunyowa ndi mame akumwamba. Zaka zisanu ndi ziwiri zidzadutsa mpaka mudzavomereze kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye mwini ulamuliro pa ma ufumu a anthu, ndipo amawapereka kwa aliyense amene Iye wafuna. Onani mutuwo |