Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 4:24 - Buku Lopatulika

24 kumasulira kwake ndi uku, mfumu; ndipo chilamuliro cha Wam'mwambamwamba chadzera mbuye wanga mfumu:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 kumasulira kwake ndi uku, mfumu; ndipo chilamuliro cha Wam'mwambamwamba chadzera mbuye wanga mfumu:

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 “Tanthauzo lake ndi ili mfumu, izi ndi zimene Mulungu Wammwambamwamba watsimikiza kuti zikugwereni mbuye wanga mfumu:

Onani mutuwo Koperani




Danieli 4:24
14 Mawu Ofanana  

Ili ndi gawo la munthu woipa, lochokera kwa Mulungu, ndi cholowa amuikiratu Mulungu.


Atsanulira chimpepulo pa akulu, nawasokeretsa m'chipululu mopanda njira.


Anazikhazikanso kunthawi za nthawi; anazipatsa chilamulo chosatumphika.


Ndidzauza za chitsimikizo: Yehova ananena ndi Ine, Iwe ndiwe Mwana wanga; Ine lero ndakubala.


Mphulupulu iomboledwa ndi chifundo ndi ntheradi; apatuka pa zoipa poopa Yehova.


Chifundo ndi ntheradi zisunga mfumu; chifundo chichirikiza mpando wake.


Yehova wa makamu wapanga uphungu uwu, kuipitsa kunyada kwa ulemerero wonse, kupepula onse olemekezeka a m'dziko lapansi.


Chitsutso ichi adachilamulira amithenga oyerawo, anachifunsa, nachinena, kuti amoyo adziwe kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu.


Pamenepo Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ake. Mfumu inayankha, niti, Belitesazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwake. Belitesazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwake kwa iwo akuutsana nanu.


Chandikomera kuonetsa zizindikiro ndi zozizwa, zimene anandichitira Mulungu Wam'mwambamwamba.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa