Danieli 4:24 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero24 “Tanthauzo lake ndi ili mfumu, izi ndi zimene Mulungu Wammwambamwamba watsimikiza kuti zikugwereni mbuye wanga mfumu: Onani mutuwoBuku Lopatulika24 kumasulira kwake ndi uku, mfumu; ndipo chilamuliro cha Wam'mwambamwamba chadzera mbuye wanga mfumu: Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201424 kumasulira kwake ndi uku, mfumu; ndipo chilamuliro cha Wam'mwambamwamba chadzera mbuye wanga mfumu: Onani mutuwo |
Pamenepo Danieli, amene amatchedwa Belitesezara, anavutika mu mtima kwambiri kwa kanthawi, ndipo anasautsidwa mʼmaganizo ake. Choncho mfumu inati, “Belitesezara usalole malotowa kapena tanthauzo lake likuopse.” Belitesezara anayankha kuti, “Mbuye wanga, ndikanakonda malotowa akanakhudza adani anu okha, ndi tanthauzo lake kwa iwo okusautsani!