Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 4:25 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Inu mudzachotsedwa pakati pa anthu ndipo mudzakhala ndi nyama zakuthengo; mudzadya udzu monga ngʼombe ndi kunyowa ndi mame akumwamba. Zaka zisanu ndi ziwiri zidzadutsa mpaka mudzavomereze kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye mwini ulamuliro pa ma ufumu a anthu, ndipo amawapereka kwa aliyense amene Iye wafuna.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

25 kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, ndipo zidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, nizidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 4:25
15 Mawu Ofanana  

Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwamba ndipo ufumu wake umalamulira onse.


Anasinthanitsa ulemerero wawo ndi fano la ngʼombe yayimuna imene imadya udzu.


Koma ndi Mulungu amene amaweruza: Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina.


Adziwe kuti Inu amene dzina lanu ndi Yehova, ndinu nokha Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi.


Ndi mphamvu zanga ndi dzanja langa lamphamvu ndinalenga dziko lapansi ndi anthu ake onse pamodzi ndi nyama zili mʼmenemo, ndipo ndimalipereka kwa aliyense amene ndikufuna.


Amasintha nthawi ndi nyengo; amakweza mafumu ndipo amawatsitsanso. Amapatsa nzeru kwa anzeru ndi chidziwitso kwa ozindikira zinthu.


Inu mfumu, ndinu mfumu ya mafumu. Mulungu wakumwamba wakupatsani ufumu, ulamuliro ndi mphamvu ndi ulemerero;


Mfumu inati kwa Danieli, “Zoonadi, Mulungu wako ndi Mulungu wa milungu ndi Ambuye wa mafumu ndi wowulula zinsinsi, pakuti iwe wathadi kuwulula chinsinsi ichi.”


Maganizo ake a umunthu asinthidwe ndipo apatsidwe maganizo a nyama ya kuthengo, mpaka zaka zisanu ndi ziwiri zitadutsa.


“ ‘Angelo oyera ndiwo akutsimikiza chilangochi. Tsono anthu adziwe kuti Mulungu Wammwambamwamba ali ndi mphamvu yolamulira maufumu onse, ndipo amawapereka kwa aliyense akumufuna, ngakhale munthu wamba kuti alamulire.’


Chandikomera kukuwuzani zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa zimene Mulungu Wammwambamwamba wandichitira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa