Danieli 4:26 - Buku Lopatulika26 Ndipo kuti anauza asiye chitsa ndi mizu ya mtengo, ufumu wanu udzakhazikikira inu, mukadzatha kudziwa kuti Kumwamba kumalamulira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201426 Ndipo kuti anauza asiye chitsa ndi mizu ya mtengo, ufumu wanu udzakhazikikira inu, mukakatha kudziwa kuti Kumwamba kumalamulira. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero26 Lamulo losiya tsinde la mtengo ndi mizu yake litanthauza kuti ufumu wanu udzabwezeredwa kwa inu mukadzavomereza kuti Mulungu ndiye amalamulira. Onani mutuwo |
Tsono, kuti mfumu inaona mthenga woyera wotsika kumwamba, ndi kuti, Likhani mtengowo ndi kuuononga, koma siyani chitsa chake ndi mizu m'nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wakuthengo, ndipo chikhale chokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama zakuthengo, mpaka zitampitira nthawi zisanu ndi ziwiri;
ndipo anamuinga kumchotsa kwa ana a anthu, ndi mtima wake unasandulika ngati wa nyama zakuthengo, ndi pokhala pake mpa mbidzi, anamdyetsa udzu ngati ng'ombe, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba; mpaka anadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, nauikira aliyense Iye afuna mwini.