Danieli 4:26 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero26 Lamulo losiya tsinde la mtengo ndi mizu yake litanthauza kuti ufumu wanu udzabwezeredwa kwa inu mukadzavomereza kuti Mulungu ndiye amalamulira. Onani mutuwoBuku Lopatulika26 Ndipo kuti anauza asiye chitsa ndi mizu ya mtengo, ufumu wanu udzakhazikikira inu, mukadzatha kudziwa kuti Kumwamba kumalamulira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201426 Ndipo kuti anauza asiye chitsa ndi mizu ya mtengo, ufumu wanu udzakhazikikira inu, mukakatha kudziwa kuti Kumwamba kumalamulira. Onani mutuwo |
“Inu mfumu munaona mthenga woyera, akuchokera kumwamba ndipo anati, ‘Gwetsani mtengo ndipo muwuwononge, koma musiye tsinde ndi mizu yake. Tsindelo mulimange ndi unyolo wa chitsulo ndi mkuwa ndipo mulisiye pakati pa udzu wa mʼmunda. Mulole kuti linyowe ndi mame akumwamba. Likhale ngati nyama zakuthengo, mpaka zaka zidutse zisanu ndi ziwiri.’
Iyo inachotsedwa pakati pa anthu ndi kupatsidwa mtima ngati wa nyama; inakhala pamodzi ndi abulu akutchire ndi kudya udzu ngati ngʼombe; ndipo thupi lake linanyowa ndi mame akumwamba, mpaka pamene anavomereza kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye wolamulira maufumu a anthu ndipo amawupereka kwa aliyense amene Iye wafuna.