Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 24:7 - Buku Lopatulika

7 nafika ku linga la Tiro ndi kumizinda yonse ya Ahivi ndi ya Akanani; natulukira kumwera kwa Yuda ku Beereseba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 nafika ku linga la Tiro ndi kumidzi yonse ya Ahivi ndi ya Akanani; natulukira kumwera kwa Yuda ku Beereseba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Ndipo adakafika ku linga la Tiro ndi ku mizinda yonse ya Ahivi, ndi ya Akanani. Atatero, adachoka kumeneko nakafika kumwera kwa Yuda, ku Beereseba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Kenaka iwo anapita molunjika linga la ku Turo ndi ku mizinda yonse ya Ahivi ndi Akanaani. Pomaliza anapita ku Beeriseba ku Negevi wa ku Yuda.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 24:7
10 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inanena ndi Yowabu kazembe wa khamu, amene anali naye, Kayendere tsopano mafuko onse a Israele, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, nuwerenge anthuwo, kuti ndidziwe kuchuluka kwao kwa anthu.


Chomwecho pamene atayenda dziko lonse anafika ku Yerusalemu pakutha miyezi isanu ndi inai, ndi masiku makumi awiri.


Ndipo Tiro adzadzimangira polimbikirapo, nadzakundika siliva ngati fumbi, ndi golide woyenga ngati thope la kubwalo.


kwa Akanani kum'mawa ndi kumadzulo, ndi kwa Aamori ndi Ahiti, ndi Aperizi ndi Ayebusi kumapiri, ndi kwa Ahivi kunsi kwa Heremoni, m'dziko la Mizipa.


ndi Ebroni, ndi Rehobu, ndi Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni wamkulu;


nazungulira malire kunka ku Rama, ndi kumzinda wa linga la Tiro; nazungulira malire kunka ku Hosa; ndi matulukiro ake anali kunyanja, kuchokera ku Mahalabu mpaka ku Akizibu;


Ndipo kunali, pakumva ichi mafumu onse a tsidya ilo la Yordani, kumapiri ndi kuchidikha, ndi ku madooko onse a Nyanja Yaikulu, pandunji pa Lebanoni: Ahiti ndi Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;


Ndipo amuna a Israele anati kwa Ahivi, Kapena mulimkukhala pakati pa ife, ndipo tipanganenji ndi inu?


anasiya mafumu asanu a Afilisti ndi Akanani onse, ndi Asidoni, ndi Ahivi okhala m'phiri la Lebanoni, kuyambira phiri la Baala-Heremoni mpaka polowera ku Hamati.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa