2 Samueli 2:13 - Buku Lopatulika13 Ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi anyamata a Davide anatuluka nakomana nao pa thamanda la Gibiyoni; nakhala pansi, ena tsidya lino, ndi ena tsidya lija la thamandalo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi anyamata a Davide anatuluka nakomana nao pa thamanda la Gibiyoni; nakhala pansi, ena tsidya lino, ndi ena tsidya lija la thamandalo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Yowabu mwana wa Zeruya pamodzi ndi ankhondo a Davide adapita kukakumana nawo ku dziŵe la Gibiyoni. Adakhala pansi, ena tsidya lina la dziŵelo, enanso tsidya lina. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Yowabu mwana wa Zeruya pamodzi ndi ankhondo a Davide anapita ndi kukakumana nawo ku dziwe la ku Gibiyoni. Gulu lina linakhala mbali ina ya dziwelo pamene gulu lina linakhala mbali inayo. Onani mutuwo |
Ndiponso udziwa chimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira, inde chimene anawachitira akazembe awiri aja a magulu a nkhondo a Israele, ndiwo Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere, amene aja anawapha, nakhetsa mwazi ngati wa nkhondo masiku a mtendere, napaka mwazi wa nkhondo pa lamba lake la m'chuuno mwake, ndi pa nsapato za pa mapazi ake.