2 Samueli 2:13 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Yowabu mwana wa Zeruya pamodzi ndi ankhondo a Davide anapita ndi kukakumana nawo ku dziwe la ku Gibiyoni. Gulu lina linakhala mbali ina ya dziwelo pamene gulu lina linakhala mbali inayo. Onani mutuwoBuku Lopatulika13 Ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi anyamata a Davide anatuluka nakomana nao pa thamanda la Gibiyoni; nakhala pansi, ena tsidya lino, ndi ena tsidya lija la thamandalo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi anyamata a Davide anatuluka nakomana nao pa thamanda la Gibiyoni; nakhala pansi, ena tsidya lino, ndi ena tsidya lija la thamandalo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Yowabu mwana wa Zeruya pamodzi ndi ankhondo a Davide adapita kukakumana nawo ku dziŵe la Gibiyoni. Adakhala pansi, ena tsidya lina la dziŵelo, enanso tsidya lina. Onani mutuwo |
“Tsono iwe ukudziwanso zoyipa zimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira pakupha atsogoleri awiri a ankhondo a Israeli, Abineri mwana wa Neri ndi Amasa mwana wa Yeteri. Iye anawapha ndi kukhetsa magazi nthawi ya mtendere ngati nthawi ya nkhondo, ndipo anapaka magazi amenewo pa lamba wa mʼchiwuno mwake ndi pa nsapato za ku mapazi ake.