2 Samueli 12:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo kwa wolemerayo kunafika mlendo, ndipo iye analeka kutengako mwa zoweta zake zazing'ono ndi zazikulu, kuphikira mlendo amene anafika kwa iye, koma anatenga mwanawankhosa wa wosaukayo, naphikira munthu amene anafika kwa iye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo kwa wolemerayo kunafika mlendo, ndipo iye analeka kutengako mwa zoweta zake zazing'ono ndi zazikulu, kuphikira mlendo amene anafika kwa iye, koma anatenga mwanawankhosa wa wosaukayo, naphikira munthu amene anafika kwa iye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Tsiku lina kunyumba kwa munthu wolemera uja kudafika mlendo. Munthu uja sadafune kutengako imodzi mwa nkhosa zake kapena imodzi mwa ng'ombe zake, kuti aphere mlendo wakeyo. M'malo mwake adakatenga nkhosa ya munthu wosauka uja, naphera mlendo amene adaadzamuchezera uja.” Atamva za munthuyo, Davide adapsa mtima kwambiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 “Ndipo mlendo anafika kwa munthu wolemera uja, koma munthu wolemerayo sanafune kutenga imodzi mwa nkhosa kapena ngʼombe zake kuti akonzere chakudya mlendo amene anafika kwa iye. Mʼmalo mwake anatenga mwana wankhosa wamkazi wa munthu wosauka uja nakonzera chakudya mlendo uja amene anabwera kwa iye.” Onani mutuwo |