Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 12:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 “Ndipo mlendo anafika kwa munthu wolemera uja, koma munthu wolemerayo sanafune kutenga imodzi mwa nkhosa kapena ngʼombe zake kuti akonzere chakudya mlendo amene anafika kwa iye. Mʼmalo mwake anatenga mwana wankhosa wamkazi wa munthu wosauka uja nakonzera chakudya mlendo uja amene anabwera kwa iye.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ndipo kwa wolemerayo kunafika mlendo, ndipo iye analeka kutengako mwa zoweta zake zazing'ono ndi zazikulu, kuphikira mlendo amene anafika kwa iye, koma anatenga mwanawankhosa wa wosaukayo, naphikira munthu amene anafika kwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo kwa wolemerayo kunafika mlendo, ndipo iye analeka kutengako mwa zoweta zake zazing'ono ndi zazikulu, kuphikira mlendo amene anafika kwa iye, koma anatenga mwanawankhosa wa wosaukayo, naphikira munthu amene anafika kwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsiku lina kunyumba kwa munthu wolemera uja kudafika mlendo. Munthu uja sadafune kutengako imodzi mwa nkhosa zake kapena imodzi mwa ng'ombe zake, kuti aphere mlendo wakeyo. M'malo mwake adakatenga nkhosa ya munthu wosauka uja, naphera mlendo amene adaadzamuchezera uja.” Atamva za munthuyo, Davide adapsa mtima kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 12:4
6 Mawu Ofanana  

koma wosaukayo analibe chilichonse kupatula kankhosa kamodzi kakakazi kamene anakagula. Iye anakasunga ndipo kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kamadya chakudya chake, kamamwera chikho chake ndipo kamagona mʼmanja mwake. Kanali ngati mwana wamkazi kwa iyeyo.


Davide anapsa mtima kwambiri chifukwa cha munthuyo ndipo anati kwa Natani, “Pali Yehova, munthu amene anachita zimenezi ayenera kufa basi!


Koma munthu aliyense amayesedwa akakokedwa ndi zilakolako zake zoyipa ndi kukopedwa nazo.


Munthu wokalamba uja anakweza maso ndipo anaona munthu wa paulendo uja atakhala pabwalo la mzindawo, ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mukupita kuti? Nanga mukuchokera kuti?”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa