2 Samueli 12:3 - Buku Lopatulika3 koma wosaukayo analibe kanthu kena koma kamwana kakakazi ka nkhosa, kamene anakagula ndi kukaweta; ndipo kameneko kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kanadyako chakudya chake cha iye yekha, kanamwera m'chikho cha iye yekha, kanagona pa chifukato chake, ndipo kanali kwa iye ngati mwana wake wamkazi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 koma wosaukayo analibe kanthu kena koma kamwana kakakazi ka nkhosa, kamene anakagula ndi kukaweta; ndipo kameneko kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kanadyako chakudya chake cha iye yekha, kanamwera m'chikho cha iye yekha, kanagona pa chifukato chake, ndipo kanali kwa iye ngati mwana wake wamkazi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Koma wosauka uja analibe nkanthu komwe kupatula kankhosa kakakazi kamodzi, kamene adaagula. Ndipo adakaŵeta kankhosako, mpaka kukula kali ndi iyeyo pamodzi ndi ana ake. Kankadyako chakudya chake cha munthuyo, mpaka kumamwera m'chikho chake. Kankagona pakhundu pake pa munthuyo, ndipo kankakhala ngati mwana wake wamkazi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 koma wosaukayo analibe chilichonse kupatula kankhosa kamodzi kakakazi kamene anakagula. Iye anakasunga ndipo kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kamadya chakudya chake, kamamwera chikho chake ndipo kamagona mʼmanja mwake. Kanali ngati mwana wamkazi kwa iyeyo. Onani mutuwo |