Kumveka kwa chikoti, ndi mkokomo wa kuyenda kwa njinga za magaleta; ndi kaphatakaphata wa akavalo, ndi gwegwegwe wa magaleta;
Yoweli 2:4 - Buku Lopatulika Maonekedwe ao aoneka ngati akavalo, nathamanga ngati akavalo a nkhondo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Maonekedwe ao aoneka ngati akavalo, nathamanga ngati akavalo a nkhondo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Maonekedwe ake ali ngati a akavalo, liŵiro lake ngati la akavalo ankhondo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Maonekedwe awo ali ngati akavalo; akuthamanga ngati akavalo ankhondo. |
Kumveka kwa chikoti, ndi mkokomo wa kuyenda kwa njinga za magaleta; ndi kaphatakaphata wa akavalo, ndi gwegwegwe wa magaleta;
Ndipo maonekedwe a dzombelo anafanana ndi akavalo okonzeka kukachita nkhondo; ndi pamitu pao ngati akorona onga agolide, ndi pankhope pao ngati pankhope pa anthu.
Pamenepo ziboda za akavalo zinaguguda. Ndi kutumphatumpha, kutumphatumpha kwa anthu ake eni mphamvu.