Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 9:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo maonekedwe a dzombelo anafanana ndi akavalo okonzeka kukachita nkhondo; ndi pamitu pao ngati akorona onga agolide, ndi pankhope pao ngati pankhope pa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo maonekedwe a dzombelo anafanana ndi akavalo okonzeka kukachita nkhondo; ndi pamitu pao ngati akorona onga agolide, ndi pankhope pao ngati pankhope pa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Dzombelo linkaoneka ngati akavalo okonzekera nkhondo. Pamitu pake panali ngati zisoti zaufumu zagolide, nkhope zake ngati za anthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Dzombe linkaoneka ngati akavalo okonzekera nkhondo. Pamitu pawo panali ngati zipewa zaufumu zagolide ndipo nkhope zawo ngati za anthu.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 9:7
6 Mawu Ofanana  

Choyamba chinanga mkango, chinali nao mapiko a chiombankhanga, ndinapenyera mpaka nthenga zake zinathothoka, ndipo chinakwezeka kudziko, ndi kuimitsidwa ndi mapazi awiri ngati munthu, ndipo chinapatsidwa mtima wa munthu.


Ndinali kulingilirira za nyangazi, taonani, pakati pa izo panaphuka nyanga ina, ndiyo yaing'ono; patsogolo pake zitatu za nyanga zoyambazi zinazulidwa ndi mizu yomwe; ndipo taonani, m'nyanga m'menemo munali maso ngati maso a munthu, ndi pakamwa palikunena zazikulu.


Ovala korona ako akunga dzombe, ndi akazembe, ndi akazembe ako ngati ziwalamsatsi zakutera m'matchinga tsiku lachisanu, koma likatuluka dzuwa ziuluka ndi kuthawa, ndi kumene zinakhalako sikudziwikanso.


Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kavalo woyera, ndipo womkwerayo anali nao uta; ndipo anampatsa korona; ndipo anatulukira wogonjetsa kuti akagonjetse.


Ndipo mu utsimo mudatuluka dzombe padziko, ndipo analipatsa ilo mphamvu monga zinkhanira za dziko zili ndi mphamvu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa