Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba; pakuti m'chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m'dziko loti see.
Yohane 5:8 - Buku Lopatulika Yesu ananena naye, Tauka, yalula mphasa yako, nuyende. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yesu ananena naye, Tauka, yalula mphasa yako, nuyende. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adamlamula kuti, “Dzuka, tenga mphasa yako, yamba kuyenda.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yesu anati kwa iye, “Imirira! Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.” |
Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba; pakuti m'chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m'dziko loti see.
Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvu Mwana wa Munthu pansi pano za kukhululukira machimo (pomwepo ananena kwa wodwalayo), Tanyamuka, nutenge mphasa yako, numuke kunyumba kwako.
Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali nayo mphamvu padziko lapansi yakukhululukira machimo, (anati Iye kwa wamanjenjeyo), Ndinena kwa iwe, Tauka, nusenze kama wako, numuke kunyumba kwako.
Ndipo Petro anati kwa iye, Eneya, Yesu Khristu akuchiritsa iwe; uka, yalula mphasa yako. Ndipo anauka pomwepo.