Yohane 4:2 - Buku Lopatulika (angakhale Yesu sanabatize yekha koma ophunzira ake), Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 (angakhale Yesu sanabatize yekha koma ophunzira ake), Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa (Komabe amene ankabatiza si Yesuyo, koma ophunzira ake). Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (ngakhale kuti Yesuyo sankabatiza, koma ophunzira ake). |
Zitapita izi anadza Yesu ndi ophunzira ake kudziko la Yudeya; ndipo pamenepo anatsotsa nao pamodzi, nabatiza.
Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Yordani, amene munamchitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa Iye.
Ndipo analamulira iwo abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Pamenepo anampempha iye atsotse masiku.