Yohane 19:3 - Buku Lopatulika nadza kwa Iye, nanena, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda! Nampanda khofu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nadza kwa Iye, nanena, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda! Nampanda khofu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa nadza kwa Iye nkumanena kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda!” Ndipo adayamba kumuwomba makofi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo ankapita kwa Iye mobwerezabwereza ndi kumanena kuti, “Moni mfumu ya Ayuda?” Ndipo amamumenya makofi. |
Ndipo analuka korona waminga, namveka pamutu pake, namgwiritsa bango m'dzanja lamanja lake; ndipo anagwada pansi pamaso pake, namchitira chipongwe, nati, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda!
Ndipo pakulowa mngelo anati kwa iye, Tikuoneni, wochitidwa chisomo, Ambuye ali ndi iwe.
Koma m'mene Iye adanena izi, mmodzi wa anyamata akuimirirako anapanda Yesu khofu, ndi kuti, Kodi uyankha mkulu wa ansembe chomwecho?
Chifukwa chake Pilato analowanso mu Pretorio, naitana Yesu, nati kwa Iye, Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda kodi?