Ambuye, chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala khunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m'madzi.
Yohane 18:2 - Buku Lopatulika Koma Yudasinso amene akampereka Iye, anadziwa malowa; chifukwa Yesu akankako kawirikawiri ndi ophunzira ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yudasinso amene akampereka Iye, anadziwa malowa; chifukwa Yesu akamkako kawirikawiri ndi ophunzira ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yudasi yemwe, amene adapereka Yesu kwa adani ake, ankaŵadziŵa malowo, pakuti Yesu ankapita kumeneko kaŵirikaŵiri ndi ophunzira ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano Yudasi, amene anamupereka amadziwa malowo chifukwa Yesu ankakumana ndi ophunzira ake kumeneko. |
Ambuye, chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala khunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m'madzi.
Ndipo usana uliwonse Iye analikuphunzitsa mu Kachisi; ndi usiku uliwonse anatuluka, nagona paphiri lotchedwa la Azitona.
Ndipo Iye anatuluka, napita monga ankachitira, kuphiri la Azitona; ndi ophunzira anamtsata Iye.