Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Yohane 12:4 - Buku Lopatulika Koma Yudasi Iskariote, mmodzi wa ophunzira ake, amene adzampereka Iye, ananena, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yudasi Iskariote, mmodzi wa ophunzira ake, amene adzampereka Iye, ananena, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Yudasi Iskariote, mmodzi mwa ophunzira a Yesu, amene analikudzampereka kwa adani ake, adati, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma mmodzi wa ophunzira ake, Yudasi Isikarioti, amene pambuyo pake adzamupereka anati, |
Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Pomwepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lake Yudasi Iskariote, anamuka kwa ansembe aakulu,
Nanga mafuta onunkhira awa sanagulitsidwe chifukwa ninji ndi marupiya atheka mazana atatu, ndi kupatsidwa kwa osauka?
Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye,
Ndipo Yesu anayankha, Ndi iyeyu, amene Ine ndidzamsunsira nthongo ndi kumpatsa. Pamenepo, m'mene anasunsa nthongo anaitenga naipatsa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote.