Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 26:14 - Buku Lopatulika

14 Pomwepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lake Yudasi Iskariote, anamuka kwa ansembe aakulu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pomwepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lake Yudasi Iskariote, anamuka kwa ansembe aakulu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Pambuyo pake Yudasi Iskariote, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja, adapita kwa akulu a ansembe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Pamenepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo wotchedwa Yudasi Isikarioti anapita kwa akulu a ansembe

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 26:14
14 Mawu Ofanana  

Simoni Mkanani, ndi Yudasi Iskariote amenenso anampereka Iye.


Ndipo Yudasi, womperekayo anayankha nati, Kodi ndine, Rabi? Iye ananena kwa iye, Iwe watero.


Ndipo Iye ali chilankhulire, onani, Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikulu la anthu, ndi malupanga ndi mikunkhu, kuchokera kwa ansembe aakulu ndi akulu a anthu.


Pamenepo Yudasi yemwe anampereka Iye, poona kuti Iye anatsutsidwa kuti afe, analapa, nabweza ndalama zija zasiliva makumi atatu kwa ansembe aakulu ndi akulu,


Koma Yudasi Iskariote, mmodzi wa ophunzira ake, amene adzampereka Iye, ananena,


Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye,


Ndipo Yesu anayankha, Ndi iyeyu, amene Ine ndidzamsunsira nthongo ndi kumpatsa. Pamenepo, m'mene anasunsa nthongo anaitenga naipatsa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote.


Pamenepo iyeyo m'mene adalandira nthongo, anatuluka pomwepo. Koma kunali usiku.


Koma Yudasinso amene akampereka Iye, anadziwa malowa; chifukwa Yesu akankako kawirikawiri ndi ophunzira ake.


Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m'kamwa mwa Davide za Yudasi, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.


(Uyutu tsono anadzitengera kadziko ndi mphotho ya chosalungama; ndipo anagwa chamutu, naphulika pakati, ndi matumbo ake onse anakhuthuka;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa