Yohane 1:8 - Buku Lopatulika Iye sindiye kuunikaku, koma anatumidwa kukachita umboni wa kuunikaku. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iye sindiye kuunikaku, koma anatumidwa kukachita umboni wa kuunikaku. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sikuti iyeyo ndiye anali kuŵalako ai, koma adangobwera kudzachitira umboni kuŵalako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iyeyu sanali kuwunika; koma anabwera ngati mboni ya kuwunika. |
Inu nokha mundichitira umboni, kuti ndinati, Sindine Khristu, koma kuti ndili wotumidwa m'tsogolo mwake mwa Iye.
Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire Iye amene adzadza pambuyo pake, ndiye Yesu.