Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 3:28 - Buku Lopatulika

28 Inu nokha mundichitira umboni, kuti ndinati, Sindine Khristu, koma kuti ndili wotumidwa m'tsogolo mwake mwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Inu nokha mundichitira umboni, kuti ndinati, Sindine Khristu, koma kuti ndili wotumidwa m'tsogolo mwake mwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Inu nomwe ndinu mboni zanga kuti ndidati, ‘Sindine Mpulumutsi wolonjezedwa uja, koma ndine wotumidwa patsogolo pake.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Inuyo ndinu mboni zanga kuti ine ndinati, ‘Ine sindine Khristu koma ndatumidwa patsogolo pa Iye.’

Onani mutuwo Koperani




Yohane 3:28
12 Mawu Ofanana  

Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.


Pakuti uyu ndiye ananenayo Yesaya mneneri, kuti, Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.


Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu; pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake.


Ndipo anavomera, wosakana; nalola kuti, Sindine Khristu.


Anati, Ndine mau a wofuula m'chipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo.


Ndipo anamfunsa iye, nati kwa iye, Koma ubatiza bwanji, ngati suli Khristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo?


ndiye wakudza pambuyo panga, amene sindiyenera kummasulira chingwe cha nsapato yake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa