anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani;
Tito 2:3 - Buku Lopatulika Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chimodzimodzinso azimai achikulire, uŵauze kuti azikhala ndi makhalidwe oyenera azimai oyera mtima. Asakhale osinjirira anzao kapena akapolo a zoledzeretsa. Akhale alangizi abwino, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chimodzimodzinso, phunzitsa amayi achikulire kuti akhale aulemu mʼmakhalidwe awo, asakhale osinjirira anzawo kapena zidakwa, koma akhale alangizi abwino. |
anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani;
kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m'zinthu zilizonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe.
Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;
Momwemonso atumiki akhale olemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, osati a chisiriro chonyansa;
Usakhalenso wakumwa madzi okha, komatu uchite naye vinyo pang'ono, chifukwa cha mimba yako ndi zofooka zako zobwera kawirikawiri.
Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati wachiwawa, wopanda ndeu, wosati wa chisiriro chonyansa;
Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna.
Komatu ndili nako kotsutsana ndi iwe, kuti ulola mkazi Yezebele, wodzitcha yekha mneneri; ndipo aphunzitsa, nasocheretsa akapolo anga, kuti achite chigololo ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano.