Yehova wa makamu wapanga uphungu uwu, kuipitsa kunyada kwa ulemerero wonse, kupepula onse olemekezeka a m'dziko lapansi.
Obadiya 1:2 - Buku Lopatulika Taona, ndakuika wamng'ono mwa amitundu; unyozedwa kwambiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Taona, ndakuika wamng'ono mwa amitundu; unyozedwa kwambiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta akuuza Aedomu kuti, “Ndithu ndidzakutsitsani kotheratu, anthu a mitundu yonse adzakunyozani kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Taona, ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina; udzanyozedwa kwambiri. |
Yehova wa makamu wapanga uphungu uwu, kuipitsa kunyada kwa ulemerero wonse, kupepula onse olemekezeka a m'dziko lapansi.
Udzakhala wopepuka wa maufumu onse, sudzadzikwezanso pa amitundu; ndipo ndidzawachepsa, kuti asachitenso ufumu pa amitundu.
Pamenepo mdani wanga adzachiona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m'miseu.
Ndi Edomu adzakhala akeake, Seiri lomwe lidzakhala lakelake, ndiwo adani ake; koma Israele adzachita zamphamvu.