Kapena Yehova adzayang'anira chosayenerachi alikundichitira ine, ndipo Yehova adzandibwezera chabwino m'malo mwa kunditukwana kwa lero.
Obadiya 1:13 - Buku Lopatulika Usalowe m'mudzi wa anthu anga tsiku la tsoka lao, kapena kupenyerera iwe choipa chao tsiku la tsoka lao, kapena kuthira manja khamu lao tsiku la tsoka lao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Usalowe m'mudzi wa anthu anga tsiku la tsoka lao, kapena kupenyerera iwe choipa chao tsiku la tsoka lao, kapena kuthira manja khamu lao tsiku la tsoka lao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kuloŵa mu mzinda wa anthu anga. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kuŵanyodola. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kulanda chuma chao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwe sunayenera kudutsa pa zipata za anthu anga pa nthawi ya masautso awo, kapena kuwanyogodola pa tsiku la tsoka lawo, kapena kulanda chuma chawo pa nthawi ya masautso awo. |
Kapena Yehova adzayang'anira chosayenerachi alikundichitira ine, ndipo Yehova adzandibwezera chabwino m'malo mwa kunditukwana kwa lero.
Ndiponso olipidwa ake ali pakati pake onga ngati anaang'ombe a m'khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao.
Popeza wanena, Mitundu iwiri iyi ya anthu ndi maiko awiri awa adzakhala anga, tidzakhala nao ngati cholowa chathu, angakhale Yehova anali komweko;
Popeza uli nao udani wosatha, waperekanso ana a Israele kumphamvu ya lupanga m'nthawi ya tsoka lao, mu nthawi ya mphulupulu yotsiriza;
Atero Ambuye Yehova, Popeza mdani ananena za inu, Ha! Ingakhale misanje yakale ili yathu, cholowa chathu;
chifukwa chake unenere, nuti, Atero Ambuye Yehova, Chifukwa, inde chifukwa kuti anakupasulani, nakumemezani pozungulira ponse, kuti mukhale cholowa cha amitundu otsala, ndipo mwafika pa milomo ya akazitape, ndi pa mbiri yoipa ya anthu;
Ndipo ndikwiya nao amitundu okhala osatekeseka ndi mkwiyo waukulu; pakuti ndinakwiya pang'ono, ndipo anathandizira choipa.