Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.
Numeri 9:17 - Buku Lopatulika Ndipo pokwera mtambo kuchokera kuchihema, utatero ana a Israele amayenda ulendo wao; ndipo pamalo pokhala mtambo, pamenepo ana a Israele amamanga mahema ao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pokwera mtambo kuchokera kuchihema, utatero ana a Israele amayenda ulendo wao; ndipo pamalo pokhala mtambo, pamenepo ana a Israele amamanga mahema ao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtambowo ukangokwera kuchoka pachihemapo, Aisraele ankanyamuka ulendo; ndipo pamene mtambowo unkakaima, Aisraele ankamanga mahema ao pamalo pamenepo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi ina iliyonse mtambo ukachoka pamwamba pa chihema, Aisraeli ankasamukanso, ndipo paliponse pamene mtambo wayima, Aisraeli ankamangapo misasa. |
Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.
Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona mu Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.
Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawachitira chifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.
Ngakhale masiku awiri, kapena mwezi, kapena masiku ambiri, pokhalitsa mtambo pamwamba pa chihema ndi kukhalapo, ana a Israele anakhala m'chigono, osayenda ulendo; koma pakukwera uwu, anayenda ulendo.
Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulumutsidwa, nadzalowa, nadzatuluka, nadzapeza busa.