Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira a zaka makumi asanu; onse akulowa kutumikira utumikiwo, kuchita ntchitoyi m'chihema chokomanako.
Numeri 8:25 - Buku Lopatulika ndipo kuyambira zaka makumi asanu azileka kutumikira utumikiwu, osachitanso ntchitoyi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo kuyambira zaka makumi asanu azileka kutumikira utumikiwu, osachitanso ntchitoyi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akafika zaka makumi asanu aleke ntchito yotumikira, ndipo asatumikirenso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma akakwana zaka makumi asanu, apume pa ntchito yawo ya tsiku ndi tsiku ndi kulekeratu kugwira ntchitoyo. |
Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira a zaka makumi asanu; onse akulowa kutumikira utumikiwo, kuchita ntchitoyi m'chihema chokomanako.
Ichi ndi cha Alevi: kuyambira ali wa zaka makumi awiri ndi zisanu ndi mphambu azilowa kutumikira utumikiwu mu ntchito ya chihema chokomanako;
koma atumikire pamodzi ndi abale ao m'chihema chokomanako, kusunga udikirowo, koma osagwira ntchito. Utere nao Alevi kunena za udikiro wao.